Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.
Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?
Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wachotsa misanje yake ndi maguwa ake a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa guwa la nsembe ili?
Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asiriya.