Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 18:16 - Buku Lopatulika

16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golide wa pa zitseko za Kachisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golide wa pa zitseko za Kachisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nthaŵi imeneyo mpamene Hezekiya adakanganula golide wa pa zitseko za Nyumba ya Chauta ndi wa pa mphuthu za makomo, amene iye yemweyo anali atamatapo. Tsono Hezekiyayo adapereka golideyo kwa mfumu ya ku Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anakanganula golide amene anakuta zitseko ndi mphuthu za chipata cha Nyumba ya Yehova namupereka kwa mfumu ya ku Asiriya.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 18:16
7 Mawu Ofanana  

Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.


Machitidwe ena tsono a Yowasi ndi zonse adazichita sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu.


Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.


Chaka choyamba cha ufumu wake, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso.


Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zake; munalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa