Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 18:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chaka chachitatu cha ufumu wa Hoseya, mwana wa Ela, mfumu ya ku Israele, Hezekiya, mwana wa Ahazi, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mʼchaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 18:1
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.


Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi mu Yerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake;


Nagona Ahazi ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Hezekiya mwana wake.


Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.


Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.


Ahazi mwana wake, Hezekiya mwana wake, Manase mwana wake,


Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mzinda wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Hezekiya analowa ufumu wake ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Abiya mwana wa Zekariya.


Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira.


Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa