Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ana a Israele anachita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'mizinda mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumzinda walinga komwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ana a Israele anachita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumudzi walinga komwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo Aisraele ankachita zinthu zoipa mobisika namachimwira Chauta Mulungu wao. Adadzimangira akachisi opembedzerako mafano ku midzi yao yonse ndi ku mizinda yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:9
10 Mawu Ofanana  

Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mzinda walinga.


ndi mtima wanga wakopeka m'tseri, ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;


Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema.


Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.


Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.


Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;


Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.


Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa