Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:7 - Buku Lopatulika

7 Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi padzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Zimenezo zidaoneka chifukwa Aisraele adachimwira Chauta Mulungu wao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, kuŵachotsa m'manja mwa Farao mfumu ya ku Ejipito. Aisraelewo ankapembedza milungu ina,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina,

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:7
27 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhale wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.


Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.


Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi mu Yerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake;


ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu ina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;


Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nachita chigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m'dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao.


Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.


Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.


Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?


Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino.


Ndinachita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.


Efuremu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wake, ndi Ambuye wake adzambwezera chomtonza chake.


Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.


Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu aakazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.


Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.


Mukalakwira chipangano cha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani.


ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvere mau anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa