Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:6 - Buku Lopatulika

6 Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Asiriya idagonjetsa Samariya, ndipo idatenga Aisraele kuŵachotsa kwao kupita nawo ku Asiriya. Idaŵakhazika ena ku mzinda wa Hala, ena kufupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndipo enanso ku mizinda ya Amedi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya, mfumu ya ku Asiriya inalanda Samariya ndipo inatenga Aisraeli ndi kupita nawo ku Asiriya. Anakawakhazika ku Hala ndi Habori mʼmbali mwa mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:6
39 Mawu Ofanana  

Ana aamuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi.


Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.


Ili kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?


Kodi milungu ya amitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?


Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.


Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m'malo mwao mpaka anatengedwa ndende.


Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.


Napeza ku Ekibatana m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, chikhale chikumbutso:


Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.


Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemisi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi? Kodi Samariya sali ngati Damasiko?


Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalira siliva, ngakhale golide sadzakondwera naye.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lake kudzaonda.


Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.


Kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu kudziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la chakudya ndi minda yampesa.


Ili kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya m'manja mwanga?


Zoonadi, Yehova, mafumu a Asiriya anaononga maiko onse, ndi pokhala pao.


Chifukwa kuti mwana asanakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.


Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse.


Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.


Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.


Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.


Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.


Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.


M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.


chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.


Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


ndikulalikirani inu lero, kuti mudzatayika ndithu, masiku anu sadzachuluka m'dziko limene muolokera Yordani kulowamo kulilandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa