Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Motero mitundu ya anthu imeneyi inkapembedza Chauta, kwinaku nkumatumikira milungu yao yachabechabe ija. Ana ao adachitanso zomwezo, adzukulu ao adachita zokhazokhazo zimene ankachita makolo ao, ndipo akuchitabe zomwezo mpaka pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Ngakhale anthuwo ankapembedza Yehova, ankatumikiranso mafano awo. Mpaka lero lino ana awo ndi zidzukulu zawo zikupitiriza kuchita zomwe ankachita makolo awo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:41
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.


Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba.


ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;


Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa