Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:40 - Buku Lopatulika

40 Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Komabe iwowo sankamva zimenezi, koma ankachitabe zimene adakhala akuchita kuyambira kale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Komabe iwo sanamvere ndipo anapitiriza kuchita zomwe ankachita kale.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:40
7 Mawu Ofanana  

natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musachita ichi.


Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele,


koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.


Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.


nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.


Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.


Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa