2 Mafumu 17:4 - Buku Lopatulika4 Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Koma tsiku lina mfumu ya ku Asiriya idaona kuti Hoseya akuchita zaupandu. Ndiye kuti Hoseyayo anali atatuma amithenga kukapempha chithandizo kwa So, mfumu ya ku Ejipito, Ndiponso adaaleka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, m'menemo kale ankakhoma chaka ndi chaka. Nchifukwa chake mfumu ya ku Asiriya itamva zimenezi, idamanga Hoseya ndi kumuika m'ndende. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Koma mfumu ya ku Asiriya inazindikira kuti Hoseya akuwukira, pakuti Hoseyayo anali atatumiza nthumwi kwa So mfumu ya Igupto ndiponso analeka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, monga ankachitira chaka ndi chaka. Choncho Salimenezeri anagwira Hoseya ndi kumuyika mʼndende. Onani mutuwo |