2 Mafumu 17:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Motero adasiya malamulo onse a Chauta Mulungu wao, nadzipangira mafano aŵiri osungunula anaang'ombe. Adapanganso mafano ena a Asera namapembedza zinthu zakumlengalenga ndiponso Baala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.