Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 17:10 - Buku Lopatulika

10 Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Adadzimangira zipilala zoimiritsa ndiponso mafano pa phiri lililonse lalitali ndi patsinde pa mitengo yogudira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Anayimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya mafano a Asera pa phiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 17:10
14 Mawu Ofanana  

Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse;


Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.


nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;


Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;


koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;


Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza ntchito ya manja aoao, imene zala zaozao zinaipanga.


Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?


Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri aatali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha mizinda yako.


Musazike kwa inu nokha mzati wa Ashera, wa mtengo uliwonse, pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.


Ndipo musamadziutsira choimiritsa chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu adana nacho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa