Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 16:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamenepo Ahazi adatuma amithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya kukanena kuti, “Ine ndine mwana wanu ndiponso mtumiki wanu. Bwerani mudzandipulumutse kwa mfumu ya ku Siriya ndi kwa mfumu ya ku Israele, amene akundithira nkhondo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ahazi anatuma amithenga kwa Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya kuti, “Ine ndine mtumiki wanu ndipo ndili pansi panu. Bwerani mudzandipulumutse mʼdzanja la mfumu ya Aramu ndiponso mʼdzanja la mfumu ya Israeli amene akundithira nkhondo.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 16:7
17 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndili nazo.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Ndipo Yehova anali naye, nachita iye mwanzeru kulikonse anamukako, napandukira mfumu ya Asiriya osamtumikira.


Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.


Nthawi yomweyo mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asiriya amthandize.


Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.


Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a achilendo.


Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako kukhala akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?


Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake.


Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo chabe; kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.


Unachitanso chigololo ndi Aasiriya, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unachita chigololo nao, koma sunakoledwe.


Anaumirira Aasiriya, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, ovala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.


Koma Ohola anachita chigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ake Aasiriya oyandikizana naye;


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa