Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 16:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya ku Israele adabwera kudzathira nkhondo Yerusalemu namzinga Ahazi ndi zithando zankhondo, koma sadathe kumgonjetsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo Rezini mfumu ya Aramu ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli anapita kukachita naye nkhondo ku Yerusalemu ndipo anazinga Ahazi, koma sanathe kumugonjetsa.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 16:5
10 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.


Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali mu Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;


Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye.


Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.


Popeza anthu awa akana madzi a Siloamu, amene ayenda pang'onopang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;


chisanavundukuke choipa chako monga nthawi ya chitonzo cha ana aakazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana aakazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa