Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 16:3 - Buku Lopatulika

3 popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma adatsata zitsanzo zoipa za mafumu a ku Israele. Adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe yopsereza potsatira miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 16:3
32 Mawu Ofanana  

panalinso anyamata ochitirana dama m'dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele.


Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.


Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.


Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israele amene adawaika.


nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.


Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake;


Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.


Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


Koma sanamvere, nawalakwitsa Manase, nawachititsa choipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israele.


Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.


Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova.


Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele.


Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


koma anasokonekerana nao amitundu, naphunzira ntchito zao:


Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto?


Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.


ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;


Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala mu Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala.


Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga?


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.


Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa