Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 16:18 - Buku Lopatulika

18 Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndipo chifukwa chofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya, adachotsa kadenga ka pamwamba pa mpando waufumu kamene anali atakamanga m'kati mwa Nyumba ya Chauta, ndiponso adatseka khomo la panja pamene mfumu inkaloŵera m'Nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Iye anachotsa kadenga ka pa Sabata kamene kanamangidwa mʼkati mwa Nyumba ya Yehova ndiponso anatseka chipata cholowera mfumu cha kunja kwa nyumba ya Yehova pofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 16:18
7 Mawu Ofanana  

ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.


Nawalamulira, kuti, Chochita inu ndi ichi: limodzi la magawo atatu la inu olowa pa Sabata lizilindira nyumba ya mfumu,


Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala.


Machitidwe ena tsono adawachita Ahazi, sanalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


amene adadikira pa chipata cha mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.


Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi.


Ndipo kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipatacho, kunja kwake, naime kunsanamira ya chipata; ndipo ansembe akonze nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, nalambire iye kuchiundo cha chipata; atatero atuluke; koma pachipata pasatsekedwe mpaka madzulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa