Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 16:16 - Buku Lopatulika

16 Nachita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Nachita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono wansembe Uriya adachita zonsezo, monga momwe mfumu Ahazi adaalamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndipo wansembe Uriya anachita monga analamulira Mfumu Ahazi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 16:16
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Uriya wansembe anamanga guwa la nsembelo, monga mwa zonse anazitumiza mfumu Ahazi zochokera ku Damasiko; momwemo Uriya wansembe analimanga asanabwere mfumu ku Damasiko.


Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Paguwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.


Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala.


Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, Mu Yerusalemu ndidzaika dzina langa.


Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, Mu Yerusalemu mudzakhala dzina langa kunthawi zonse.


Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.


Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu.


Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa