2 Mafumu 16:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Pamene mfumu Ahazi adapita ku Damasiko kuti akakumane ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adaonako guwa kumeneko. Tsono adatumizira wansembe Uriya chitsanzo chake cha guwalo ndi maonekedwe ake, osasiyapo nkanthu komwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Kenaka mfumu Ahazi inapita ku Damasiko kukakumana ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya. Iye anaona guwa lansembe ku Damasiko kuja ndipo anatumiza chitsanzo chake kwa wansembe Uriya, osasiyapo nʼkanthu komwe kuti athe kulimanga. Onani mutuwo |
Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite.