Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:8 - Buku Lopatulika

8 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele mu Samariya miyezi isanu ndi umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chaka cha 38 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu, adaloŵa ufumu wa Aisraele ku Samariya kwa miyezi isanu ndi umodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mʼchaka cha 38 cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira miyezi isanu ndi umodzi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:8
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.


Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.


Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Zekariya mwana wake.


Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi mu Samariya.


Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi mu Samariya.


Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.


Nagona Azariya ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Yotamu mwana wake.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.


ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa