Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:4 - Buku Lopatulika

4 Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Komabe malo opembedzerako mafano sanawachotse ndipo anthu anapitirizabe kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:4
12 Mawu Ofanana  

Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.


Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.


Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya.


Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.


Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.


Ndi mtima wake unakwezeka m'njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo mu Yuda.


Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?


Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa