Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:23 - Buku Lopatulika

23 Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Chaka cha 50 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Mʼchaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka ziwiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:23
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Nadabu mwana wa Yerobowamu analowa ufumu wa Israele chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa analowa ufumu wa Israele ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.


Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Pekahiya mwana wake.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.


Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele mu Samariya miyezi isanu ndi umodzi.


Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka ziwiri mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.


kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa