Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:17 - Buku Lopatulika

17 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi mu Samariya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Chaka cha 39 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Menahemu mwana wa Gadi adaloŵa ufumu wa ku Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ku Samariya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Mʼchaka cha 39 cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira mu Samariya zaka khumi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:17
6 Mawu Ofanana  

Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi mu Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.


Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele mu Samariya miyezi isanu ndi umodzi.


Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa