Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:16 - Buku Lopatulika

16 Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nthaŵi imeneyo, kuchokera ku Tiriza Menahemu adakaononga mzinda wa Tapuwa ndi anthu onse amene anali m'menemo, kuphatikiza dziko lonse lozungulira, poti iwo sadamgonjere. Adaphanso akazi apathupi amumzindamo naŵang'amba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Nthawi imeneyo Menahemu, kuchokera ku Tiriza, anakathira nkhondo mzinda wa Tipisa ndi anthu onse amene anali mʼmenemo ndi dera lonse lozungulira chifukwa iwo anakana kutsekula zipata zawo. Iye anatenga katundu yense mu mzinda wa Tipisa ndi kutumbula akazi onse oyembekezera.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:16
6 Mawu Ofanana  

Pakuti analamulira dziko lonse lili tsidya lino la Yufurate, kuyambira ku Tifisa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya lino la Yufurate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko.


Machitidwe ena tsono a Salumu ndi chiwembu chake anachichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.


Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.


Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;


Ndipo Abimeleki anafika kunsanja, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa