Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 15:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono Salumu mwana wa Yabesi adamchita chiwembu Zekariya, ndipo adamphera ku Ibleamu. Choncho Salumuyo adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Salumu mwana wa Yabesi anachitira chiwembu Zekariya. Anamukantha anthu akuona, namupha, ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 15:10
16 Mawu Ofanana  

Inde Baasa anamupha chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwake.


Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m'mzinda wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo anamchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.


Machitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.


Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi mu Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.


Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Pekahiya mwana wake.


Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye mu Samariya, m'nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


Yehu anakoka uta wake ndi mphamvu zonse, nalasa Yoramu pachikota, nupyoza muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m'galeta wake.


Ndipo polowa Yehu pachipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimiri, iwe wakupha mbuyako?


Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.


Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.


ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa