Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 14:9 - Buku Lopatulika

9 Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama yakuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udaatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pomwepo, nkuupondereza mtungwiwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma Yehowasi mfumu ya Israeli anabweza mawu kwa Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Mtengo wa minga wa ku Lebanoni unatumiza uthenga kwa mkungudza wa ku Lebanoni. ‘Patse mwana wako wamkazi kuti ndimukwatire.’ Kenaka chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa mingawo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 14:9
15 Mawu Ofanana  

Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikira hisope wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.


Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi.


Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.


(pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate; ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.)


Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho.


Monga munga wolasa dzanja la woledzera, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.


Ngati kakombo pakati pa minga momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.


Ndipo minga idzamera m'nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m'malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.


Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.


Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?


Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa