Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 14:7 - Buku Lopatulika

7 Anapha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Anapha Aedomu m'Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono Amaziya adaphanso Aedomu okwanira 10,000 ku chigwa cha Mchere, nalanda mzinda wa Sela, ndipo adautchula dzina lakuti Yokitele, ndipo dzina lake ndi lomwelo mpaka pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iye ndiye amene anapha Aedomu 10,000 mʼchigwa cha Mchere nalanda mzinda wa Sela pa nkhondo ndipo anawutcha Yokiteeli, dzina lake ndi lomwelo mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 14:7
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anamveketsa dzina lake pamene anabwera uko adakantha Aaramu mu Chigwa cha Mchere, ndiwo anthu zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.


Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.


Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;


Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.


Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.


Tumizani inu anaankhosa kwa wolamulira wa dziko kuchokera ku Sela kunka kuchipululu, mpaka kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?


ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa