Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 14:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono Amaziya adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati nthaŵi zonse monga Davide kholo lake. Ankachita zonse monga m'mene ankachitira Yowasi bambo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi zomwe anachita Davide kholo lake. Iye anatsatira zochita zonse za Yowasi abambo ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 14:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhale wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.


Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake.


Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.


Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.


Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.


Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai mu Yerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake.


Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.


Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.


Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa