Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 14:20 - Buku Lopatulika

20 Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Tsono adamtengera pa akavalo, nakamuika ku Yerusalemu m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Anabwera naye ku pa kavalo ku Yerusalemu ndi kumuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 14:20
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide.


Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m'mzinda wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo anamchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.


Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.


Nagona Yoramu ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo anyamata ake anamnyamulira pagaleta kunka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ake pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide.


Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.


Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa