2 Mafumu 14:14 - Buku Lopatulika14 Natenga golide ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m'nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Natenga golide ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m'nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Pamenepo adalanda golide ndi siliva yense, ndi ziŵiya zonse zimene adazipeza m'Nyumba ya Chauta ndi m'nyumba zosungira chuma cha mfumu. Adagwiranso anthu ena ngati chikole, nabwerera ku Samariya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Iye anatenga golide ndi siliva yense pamodzi ndi ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndi zimene zinali mosungira chuma cha nyumba ya mfumu. Iye anagwiranso anthu nabwerera ku Samariya. Onani mutuwo |
Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,
Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.