2 Mafumu 13:6 - Buku Lopatulika6 Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; nichitsalanso chifanizo m'Samariya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Komabe Aisraelewo sadaleke kuchita zoipa zimene ankazichita anthu a pa banja la Yerobowamu, zimene iye ankachimwitsa nazo Aisraele. Aisraele adachitabe zoipazo, ndipo fano la Asera nalonso lidakhalabe ku Samariya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Komabe Aisraeli sanaleke kuchita machimo a nyumba ya Yeroboamu, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iwo anapitirira kuchita machimowo. Ndiponso fano la Asera linakhalabe ku Samariya. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.