Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi padzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi pa dzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Nchifukwa chake Chauta adasankha mtsogoleri kuti apulumutse Aisraele m'manja mwa Asiriya. Motero Aisraele adakhala mwamtendere m'dziko mwao, monga momwe ankakhalira kale.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova anapatsa Aisraeli munthu woti awapulumutse ndipo anapulumuka mʼdzanja la Aramu. Choncho Aisraeli anakhala mʼnyumba zawo monga ankachitira kale.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:5
13 Mawu Ofanana  

Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele mizinda ija adailanda m'dzanja la Yehowahazi atate wake ndi nkhondo. Yehowasi anamkantha katatu, naibweza mizinda ya Israele.


Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.


Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.


Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.


Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.


Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi.


Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.


Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.


Ndipo apulumutsi adzakwera paphiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova.


pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.


Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse;


Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.


Pamenepo Yonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Yonatani anafika naye Davide kwa Saulo, iye nakhalanso pamaso pake monga kale.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa