Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:4 - Buku Lopatulika

4 Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono Yehowahazi adapemphera kwa Chauta ndipo Chauta adamumvera, poti adaona kupsinjidwa kwa Aisraele kumene mfumu ya ku Siriya idaŵapsinja nako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:4
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.


Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.


Ndipo Hazaele mfumu ya Aramu anapsinja Israele masiku onse a Yehowahazi.


Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.


Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.


Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.


Momwemo tinasala ndi kupempha ichi kwa Mulungu wathu; nativomereza Iye.


Udzampemphera ndipo adzakumvera; nudzatsiriza zowinda zako.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.


Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;


Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.


Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.


Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zopambana, zimene suzidziwa.


Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa