Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:18 - Buku Lopatulika

18 Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndipo adati, “Tengani mivi inayo.” Yehowasi adaitenga. Tsono Elisa adauza mfumu ya ku Israele ija kuti, “Lasani pansi miviyo.” Ndipo iye adalasa pansi katatu, nkuleka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:18
9 Mawu Ofanana  

Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu mu Afeki mpaka mudzawatha.


Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.


Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele mizinda ija adailanda m'dzanja la Yehowahazi atate wake ndi nkhondo. Yehowasi anamkantha katatu, naibweza mizinda ya Israele.


Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.


Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele anapambana; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke anapambana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa