Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Motero Yehowasi adamwalira, naikidwa ku Samariya pamodzi ndi mafumu a ku Israele. Tsono Yerobowamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Yowasi anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo Yeroboamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yowasi anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:13
12 Mawu Ofanana  

Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa.


Nati kwa Yerobowamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Taona ndidzaung'amba ufumu m'dzanja la Solomoni ndi kukupatsa iwe mafuko khumi.


Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide.


Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!


Ndipo Yehowahazi anagona ndi makolo ake, namuika mu Samariya; nakhala mfumu m'malo mwake Yowasi mwana wake.


Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.


Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa