Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:12 - Buku Lopatulika

12 Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene adazichita, kudzanso zamphamvu zimene adaonetsa pomenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:12
8 Mawu Ofanana  

Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.


Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.


Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele.


Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa