Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:11 - Buku Lopatulika

11 Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nayenso adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanaleke kuchita tchimo la Yeroboamu mwana wa Nebati limene anachimwitsa nalo Israeli.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:11
6 Mawu Ofanana  

Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang'ombe agolide okhala mu Betele ndi mu Dani.


Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi.


Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.


Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya.


Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa