2 Mafumu 12:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi paguwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi pa guwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Tsono wansembe Yehoyada adatenga bokosi, ndipo adaboola chivundikiro chake, naika bokosilo pambali pa guwa cha ku dzanja lamanja kwa aliyense woloŵa m'Nyumba ya Chauta. Ansembe amene anali pa khomo ankaponyamo ndalama zonse zimene anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.