Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 12:8 - Buku Lopatulika

8 Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Motero ansembe aja adavomera kuti sadzatenganso ndalama kwa anthu, ndipo kuti sindiwo adzakonza Nyumbayo, koma ena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 12:8
4 Mawu Ofanana  

Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.


Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi paguwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova.


Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova,


Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja kuchipata cha nyumba ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa