Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 12:7 - Buku Lopatulika

7 Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nchifukwa chake mfumu Yowasi adaitana wansembe Yehoyada ndi ansembe ena, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza Nyumbayi? Kuyambira tsopano, musasungenso ndalama za anthu amene mumaŵatumikira, koma muzipereke kuti akonzere Nyumbayi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 12:7
9 Mawu Ofanana  

Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.


Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.


Koma kunali, chaka cha makumi awiri mphambu zitatu cha mfumu Yowasi, ansembe sanathe kukonza mogamuka nyumba.


Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba.


Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?


Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.


Ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino mu Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.


Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa