Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 12:12 - Buku Lopatulika

12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ankalipiranso amisiri omanga ndi miyala ndi osema miyala, ndiponso ankagula mitengo ndi miyala yokumba yokonzera Nyumba ya Chauta, kudzanso zinthu zina zilizonse zofunikira poikonza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 amisiri a miyala ndiponso anthu ophwanya miyala. Iwo ankagula matabwa ndi miyala yosema yokonzera Nyumba ya Yehova ndipo ankalipira zinthu zonse zofunika pokonzanso nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 12:12
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;


Napereka ndalama zoyesedwa m'manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova,


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, ndi kuikidwa mitengo pamakoma, ndipo inachitika mofulumira ntchitoyi, ndipo inayenda bwino m'dzanja mwao.


Ndipo pamene ena analikunena za Kachisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati Iye,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa