Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 12:1 - Buku Lopatulika

1 Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Yehu, Yowasi adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka makumi anai ku Yerusalemu. Mai wake anali Zibiya wa ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka makumi anayi. Amayi ake anali Zibiya wa ku Beeriseba.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 12:1
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.


Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.


Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.


Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi.


Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.


Yoramu mwana wake, Ahaziya mwana wake, Yowasi mwana wake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa