2 Mafumu 11:2 - Buku Lopatulika2 Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, adatenga Yowasi, mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero adamubisa mwanayo, kubisira Ataliya, kotero kuti sadaphedwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe. Onani mutuwo |
Koma Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wake m'chipinda chogonamo. Momwemo Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wake wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.