2 Mafumu 11:18 - Buku Lopatulika18 Namuka anthu onse a m'dzikomo kunyumba ya Baala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Namuka anthu onse a m'dzikomo kunyumba ya Baala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Choncho anthu onse a m'dzikomo adapita ku nyumba ya Baala nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenako adapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Tsono wansembe Yehoyada adaika alonda ku Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya ukapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.