Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 11:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m'manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m'manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono adandanditsa asilikaliwo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi zida m'manja mwake, kuzungulira guwalo ndiponso Nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 11:11
9 Mawu Ofanana  

Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.


Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.


Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m'manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye.


Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake.


Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.


Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.


Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?


kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.


kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa