2 Mafumu 10:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo kunali m'mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo kunali m'mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 M'maŵa mwake atatuluka, Yehu adapitako nauza anthu onse kuti, “Inu sindinu ochimwa ai. Wochimwa ndine, popeza kuti ndidachita chiwembu mbuyanga, ndipo ndidamupha. Koma adapha anthu onseŵa ndani? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Mmawa mwake Yehu anatuluka. Iye anayimirira pamaso pa anthu onse ndipo anati, “Inu ndinu osalakwa. Ndine amene ndinachita chiwembu mbuye wanu ndi kumupha, koma kodi wapha anthu onsewa ndani? Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.