Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndiye akuluakuluwo atalandira kalata ija, adagwira zidzukulu za mfumuzo nkuzipha, 70 zonsezo, naika mitu yao m'madengu, nkuitumiza kwa Yehu ku Yezireele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kalatayo itafika, anthuwo anatenga ana a mfumu 70 aja ndi kuwapha onse. Anayika mitu yawo mʼmadengu ndi kuyitumiza ku Yezireeli kwa Yehu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:7
9 Mawu Ofanana  

Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.


Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele;


Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mzinda, amene anawalera.


Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu ya ana a mfumu. Nati iye, Muiunjike miulu iwiri polowera pa chipata kufikira m'mawa.


Ndipo kunali m'mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?


Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.


Atauka tsono Yehoramu mu ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa