2 Mafumu 10:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mzinda, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Motero woyang'anira nyumba ya mfumu ndiponso wina woyang'anira mzinda, pamodzi ndi akuluakulu, kudzanso amene ankalera anawo, adatumiza mau kwa Yehu kuti, “Ife ndife anthu anu, ndipo tidzachita zonse zimene mutiwuze. Sitidzaika wina aliyense kuti akhale mfumu. Muchite zonse zimene zikukomereni.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, bwanamkubwa wa mzinda, akuluakulu ena ndiponso olera anawo anatumiza uthenga uwu kwa Yehu: “Ife ndife atumiki anu ndipo tidzachita chilichonse chomwe mutiwuze. Sitidzasankha munthu wina aliyense kukhala mfumu ndipo chitani chimene mukuganiza kuti nʼchabwino kwa inu.” Onani mutuwo |