Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Ndipo Chauta adauza Yehu kuti: “Chifukwa choti wachita zondikomera Ine, poononga banja la Ahabu monga momwe ndinkafunira, ana ako adzakhala pa mpando waufumu wa Israele mpaka mbadwo wachinai.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Yehova anati kwa Yehu, “Chifukwa wachita bwino pokwaniritsa kuchita zabwino pamaso panga ndipo wachitira banja la Ahabu zonse zimene zinali mʼmaganizo anga, zidzukulu zako zidzakhala pa mpando waufumu wa Israeli mpaka mʼbado wachinayi.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:30
13 Mawu Ofanana  

Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ake.


ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.


Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.


Nagona Yehu ndi makolo ake, namuika mu Samariya. Ndi Yehowahazi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.


Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi.


Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.


Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Zekariya mwana wake.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.


Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa