Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:23 - Buku Lopatulika

23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Yehu adaloŵa m'nyumba ya Baala pamodzi ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu. Ndipo adauza anthu aja opembedza Baalaŵa kuti: “Yang'anani bwino, ndipo muwone kuti pasakhale mtumiki wa Chauta pano pakati panupa, koma opembedza Baala okhaokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Kenaka Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu analowa mʼnyumba ya Baala. Yehu anawawuza atumiki a Baala kuti, “Yangʼanitsitsani ndipo muone kuti muno musapezeke atumiki a Yehova, koma mukhale atumiki okhawo a Baala.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:23
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;


Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala.


Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake.


Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kwamuyaya;


Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.


Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa