Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Yehu adatumiza mau ku dziko lonse la Israele, ndipo onse amene ankapembedza Baala adabweradi, kotero kuti sadatsalepo ndi mmodzi yemwe. Onsewo adaloŵa m'nyumba ya Baala, ndipo anthu adachita kuti thothotho m'nyumbamo. Sipadatsale malo mpang'ono pomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Pamenepo Yehu anatumiza mawu ku dziko lonse la Israeli ndipo atumiki onse a Baala anabwera; palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala. Iwo anadzaza nyumba ya Baala. Nyumbayo inadzaziratu kuchokera ku khoma lina mpaka ku khoma lina.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:21
7 Mawu Ofanana  

Nammangira Baala guwa la nsembe m'nyumba ya Baala anaimanga mu Samariya.


Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala.


Namuka anthu onse a m'dzikomo kunyumba ya Baala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova.


ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa.


Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa mu Chihebri Armagedoni.


Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samisoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa