Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:11 - Buku Lopatulika

11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pambuyo pake Yehu adapha onse otsala a banja la Ahabu ku Yezireele, akuluakulu ake onse, abwenzi ake onse ozoloŵerana naye ndiponso ansembe ake. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Choncho Yehu anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Yezireeli, pamodzinso ndi akuluakulu ake onse, abwenzi ake ndiponso ansembe ake, sanasiyeko ndi mmodzi yemwe wamoyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:11
25 Mawu Ofanana  

chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka mu Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse.


Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo;


Ndipo kunali, atalowa ufumu wake, nakhala pa mpando wachifumu wake, anawakantha onse a m'nyumba ya Baasa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ake, kapena wa mabwenzi ake.


Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.


Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.


ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele.


Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.


Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Pamenepo ananyamuka, nachoka, namuka ku Samariya. Ndipo pokhala kunyumba yosengera ya abusa panjira,


Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.


Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele.


Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya.


Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.


Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Yuda, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.


Sadzakhala naye mwana kapena chidzukulu mwa anthu a mtundu wake, kapena wina wotsalira kumene anakhalako.


Zidzukulu zake zidulidwe; dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.


Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.


ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yake m'dzanja la Israele; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namchitira mfumu yake monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.


Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.


ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa